Yemwe akufuna kudzayimira nawo pa udindo wa mtsogoleri wa dziko, Milward Tobias, wati kuthetsa ndalenza zipani ndi njira imodzi yomwe ingathandize potukula dziko lino.
Tobias wati ndi chifukwa chake iye akufuna kudzayimira nawo pa mpandowu posayimira chipani chilichonse.
“Ine Milward Tobias ndidzaima pa udindo wa mtsogoleri wa dziko chisankho cha pa 16 September chaka chino. Ndakhala ndikufotokoza izi kuyambira September 2022. Ndakhala ndikunena kuti tikufunika kusintha kachitidwe ka ndale kuti kusintha kwenikweni kwa chuma cha dziko ndi kutukula miyoyo ya anthu kutheke. Dziko lino lakhala likusintha nkhope za atsogoleri ndi chipani cholamula omwe apitiriza ndale zozunza ndi kusaukitsa a Malawi. Pakufunika tichotse ndale za chipani ndi kuchotsa njira zokopa anthu kugwiritsa ntchito nsalu, ma t-shirt, zipewa ndi ndalama zimene zimafuna ndalama zambiri zomwe ochita ndalewo alibe. Ndiye amakatichititsa pinyolo kwa zigawenga kumene amakatenga ndalama zogulira zimenezo kuti akayikidwa pa mpando ikhale nthawi yobweza,” iye anatero pocheza ndi mtolankhaniyu Lolemba.
Tobias adati ndi zomvetsa chisoni kuti ndalama za boma zimene zikadatukula miyoyo yathu zimakabweza kwa zimene amatenga nthawi ya misonkhano yokopa anthu.
Iye wati ndi wokonzeka kubweretsa kusintha kwenikweni ndi cholinga choti atumikire aMalawi mowona mtima, poonetsetsa kuti ndalama iliyonse ya boma ikagwire ntchito yotukula miyoyo ya anthu.
“Pasadzakhale gulu lomamva kuti boma ndi lawo kuposa anthu ena chifukwa chipani chawo ndiye chikulamula. Ine ndidzaima ngati independent kuti ndikatumikire a Malawi nonse chimodzimodzi. Aliyense adzakhala ndi mwayi ofanana kupeza ntchito ku boma, ngongole ku NEEF komanso kuthandizidwa ndi boma lake mogwirizana ndi kuthekera kwake kapena zosowa zake chifukwa ndi nzika ya Malawi,” anatsindika chonchi.
Zina zomwe adanena ndi izi:
Anthu amene alembetsa kudzavota ndi 7.2 million. Potengera lamulo lakuti opambana apeze mavoti opitirira theka, tikufuna mavoti opitirira 3.6 million kuti tipambane chisankhochi popanda kuvotanso kachiwiri patatha masiku 60. Choncho, ndikukufikirani kuti mukhale mbali yosintha kwenikweni ndikutsogoleraku. Pempho langa ndi lakuti mukhale marketing campaign supervisor kwa abwenzi and abale anu onse. Chisankho ichi si masewero a mpira amene abambo atha kukhala a timu ina, amai timu inanso ndi mwana timu inanso yosiyana. Chisankho ichi si chapakati pa mtundu wina ndi unzake, kapena chigawo china ndi chinzake, kapena chipembedzo china ndi chinzake. Chisankho ichi ndi pakati pa umphawi ndi chitukuko, katangale ndi ungwiro, kubwerera mbuyo ndi kupita mtsogolo. Choncho ngati mwachita chiganizo chodzandivotera, senzani udindo wotsimikizira aliyense amene mumadziwana naye kuti adzandivoterenso.
Mmalo modera nkhawa kuti uthenga ndiwufikitsa bwanji kwa anthu onse, dziwoneni inuyo kukhala mbali yofikitsa uthengawo kwa anthu onse.
Tangoganizani anthu 10,000 okha aliyense atatsimikizira anthu osachepera 300 ena, ndiye kuti takwanitsa kale mavoti 3 million. Ndikudziwa inu mungathe kutsimikizira anthu oposa pamenepa mwinanso mudzi onse chifukwa cha mmene mumakhalira bwino ndi anthu. Tiyeni tibweretse kusintha limodzi. Tengani mbali.
Tumizirani anzanu uthengawu ngati mbali imodzi yokwaniritsa pempholi.
Mulungu akudalitseni. Salaam Alaikum. Zikomo kwambiri
Follow and Subscribe Nyasa TV :