LILONGWE-(MaraviPost)-Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera wachenjeza kuti achotsa ntchito nduna zonse zosagwira bwino ntchito.
Poyankhura ku msonkhano omwe amachititsa pa sukulu ya sekondale ya Malembo ku Lilongwe, Chakwera wachenjezanso akuluakulu ena a boma kuti sasekelera chibwana cha mtundu wina ulionse.
“Chifukwa ndikudziwa kuti m’maundunamu m’mapezeka timadailekitala tina tochitira mwano mabwana awo. Tomanena kuti iwowo a PS sangawauze zochita kaamba koti amadziwana ndi anduna, Chief of Staff kapena ma advisor ku State House, sindifuna chibwana cha mtundu umenewoyi.
“Ena nde kumachita kunena kuti ndimadziwana ndi Pulezidenti… Chibwana chimenecho chatha… Muchotsedwera limodzi,” waopseza motero Chakwera.
Pomaliza, Dr Chakwera wati: “Mulungu salakwitsa ndipo sanatiike m’boma kuti tilephere. koma tilikutumukirani ndipo n’zotheka.
Discover extra from The Maravi Post
Subscribe to get the most recent posts despatched to your e mail.